Mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education NICE wa m’boma la Ntchisi a Adam Disi ati bungwe lawo ndilokozeka kuphuzitsa anthu onse okhudzidwa za ubwino ochita ndale mwa bata.
Iwo anati ngati bungwe la NICE akhala akuchititsa misonkhano ndi adindo komanso anthu onse m’bomali pofuna kuwonetsetsa kuti tidzakhale ndi chisankho cha mtendere pa 16 September 2025.
“Ife tikhala tikuyenda mumisika komanso tikumana ndi adindo osiyanasiyana pofuna kufalitsa uthenga wakuti pasankhale ziwawa pa ndale” anatero a Disi.
Pogwilizana ndi a Disi mfumu yayikulu Kalumo ya m’bomali yati yayamba kale kukumana ndi mafumu kuwadziwitsa za udindo wawo pofuna kuti chisankho chikubwelachi chidzakhale cha Mtendere.
Iwo alankhula izi lero mu pologilamu yapandera yomwe bungwe la NICE linakoza pawailesi ya Ntchisi Youth FM ndipo mu programyi munalinso a Sub-Inspector Mzembe kuchokera ku polisi ya Ntchisi ndi a Mwawonanji Kachisuzi yemwe ndi mkhalapampando wa achinyamata m’boma la Ntchisi.
Olemba : Chifuniro Chikaphonya (27 March 2025)
NY FM mphanvu kwa mzika