Home Uncategorized Phungu wakumwera m’boma la Ntchisi a Ulemu Chilapondwa lero akawonekera ku komiti yayikulu ya chipani cha Malawi Congress Party MCP ya m’bomali powonetsa chidwi choyima nawo pachisankho chachipulura chomwe chichitike posachedwapa.

Phungu wakumwera m’boma la Ntchisi a Ulemu Chilapondwa lero akawonekera ku komiti yayikulu ya chipani cha Malawi Congress Party MCP ya m’bomali powonetsa chidwi choyima nawo pachisankho chachipulura chomwe chichitike posachedwapa.

by Clary Simion
0 comments

Polankhula atalandilidwa phunguyu anati ndiwokondwa kuti chipani chamulandila mwasangala iwo anawonjezera kuti akapanga kampeni yabata kuti akapambane pachisankho chachipulura ndikudzayima patikiti ya chipanichi.

A Chilapondwa anatinso agwira ntchito usana ndi usiku kuthandizila kuti mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress Party MCP, Dr Lazarus Chakwera adzapambane pachisankho chapa 16 September 2025 ponena kuti zitha kukhala zopweteka ngati phungu atapambana koma mtsogoleri osapambana.

Kumbali yake mkhalapampando wakomiti ya chipanichi m’bomali a James Chibade analimbikitsa a Chilapondwa kuti akapange kampeni yabata ndikuuza anthu zokhazo zomwe zingabweletse pamodzi anthu m’bomali ndikuti anthandizile kuti chipanichi chidzapambane pamasankho cha pa 16 September 2025.

Phunguyu wakhala oyamba kukawonekera kuchipanichi mwa a phungu onse anayi omwe ali m’bomalo.

Olemba: Chifuniro Chikaphonya ( 15 April 2025)
NY FM mphanvu kwa mzika

You may also like

Leave a Comment

Dowa Community Radio is a community-based radio station established in 2020 to be used as a tool of communication in Dowa district and surrounding areas to facilitate issues of Education, gender-based violence, culture, child trafficking, Agriculture, Climate change and environment, transparency and accountability, sports, community self reliance, and many more.

Newsletter

Subscribe my Newsletter for new blog posts, tips & new photos. Let's stay updated!

@2025 – All Right Reserved. MACRA Community Radios

Are you sure want to unlock this post?
Unlock left : 0
Are you sure want to cancel subscription?
-
00:00
00:00
Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00