M’mawu ake mkulu oyang’anira nkhani za uchembere komanso ubereki wabwino ku bungwe la MAMU a Francis Nyasulu, wati bungwe lawo linachiona chinthu cha mtengo wapatali kubweretsa adindo osiyanasiyana pofuna kulimbikitsa achinyamata kuti azitha kupita kukayesetsa magazi kuti azidziwa m’mene mthupi mwawo muliri.
“Ngati bungwe ena mwamavuto omwe tikukumana nawo ndikusowekela kulumikizana kwabwino maka kwa adindo ogwira ntchito kuchipatala pakugawana kwamauthenga kuti achinyamata azitha kuthandizika mosavuta”,anatero Nyasulu.
Poyankhula Mmodzi mwa achinyamata a Happiness Kapangama ochokela kwa T/A chilooko m’boma la Ntchisi ati mkumanowu uthandizira achinyamata kutula khawa zawo zosiyanasiyana zomwe amakumana nazo pa khani zauchembere wabwino ndi ubereki komanso adzifotokozelana khani zimenezi momasuka.
Bungwe La Muslim Association of Malawi likugwila ntchito ndi achinyamata m’boma la Ntchisi
ndikuwalimbikitsa kuti azitha kumatenga njira zakulera monga ngati Macondom komanso mapills.
Ntchitoyi ikutchedwa mzatonse pulojekiti ndi nthandizo la ndalama kuchokera ku Boma la Germany kudzera ku KFW bank.
Wolemba:Joy Mapulanga
(20 June 2025)
NYFMmphanvukwamzika

