Iwo anati boma la a Chakwera lachita zitukuko zambili monga kumanga misewu,kumanga zipinda zophuziliramo komanso kumanga nyumba za apolisi kungotchulako zochepa chabe.
Poyankha pa zomwe a Traditional Authority Kalumo anapempha a Chimwendo anati Boma layika kale ndalama zambili mu budget ya chaka cha 2025 kufika 2026 zomwe zithandize kuti amalawi asafe ndi njala komanso feteleza abwera ochuluka kuti anthu akalimire kudimba.
Iwo amalankhula izi pa msonkhano wa ndale omwe chipani cha Malawi Congress Party MCP chinachititsa pa Makanda primary school ground m’boma la Ntchisi komwenso ndikudera la olemekezeka a Ulemu Chilapondwa.
Olemba: Chifuniro Chikaphonya (13 April 2025)
NY FM mphanvu kwa mzika

