Iwo anati nthawi yomwe anayendetsa dziko lino zinthu zinali pabwino pomwe wati nthawi yake anagawa ng’ombe,kubwezeletsa Chuma mchimake,kugawa njinga zamoto komanso anthu samagona ndi njala zomwe wati nthawi yakwana kuti anthu amuyike pampando pakuti kagwilidwe kantchitoyi akuyidziwa.
Ndipo iwo ati adziwonera okha pomwe amabwela kuti chimanga m’minda mulibe zomwe zikusonyezelatu kuti m’boma la Ntchisi kukhala njala yadzawoneni.
Olemba: Chifuniro Chikaphonya (06 April 2025)
#NY FM mphanvu kwa mzika#