Polankhula atalandilidwa phunguyu anati ndiwokondwa kuti chipani chamulandila mwasangala iwo anawonjezera kuti akapanga kampeni yabata kuti akapambane pachisankho chachipulura ndikudzayima patikiti ya chipanichi.
A Chilapondwa anatinso agwira ntchito usana ndi usiku kuthandizila kuti mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress Party MCP, Dr Lazarus Chakwera adzapambane pachisankho chapa 16 September 2025 ponena kuti zitha kukhala zopweteka ngati phungu atapambana koma mtsogoleri osapambana.
Kumbali yake mkhalapampando wakomiti ya chipanichi m’bomali a James Chibade analimbikitsa a Chilapondwa kuti akapange kampeni yabata ndikuuza anthu zokhazo zomwe zingabweletse pamodzi anthu m’bomali ndikuti anthandizile kuti chipanichi chidzapambane pamasankho cha pa 16 September 2025.
Phunguyu wakhala oyamba kukawonekera kuchipanichi mwa a phungu onse anayi omwe ali m’bomalo.
Olemba: Chifuniro Chikaphonya ( 15 April 2025)
NY FM mphanvu kwa mzika